Deuteronomy 5:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iwe Mose, ukhale kuno pamodzi ndi Ine, ndipo ndidzakupatsa malamulo, malangizo ndi zina zoyenera kuzitsata. Zonsezi ukaŵaphunzitse anthu kuti azikasunga malamulowo m'dziko limene ndidzaŵapatsalo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iwe, uime kuno ndi Ine, ndinene ndi iwe malamulo onse, ndi malamba, ndi maweruzo, amene uziwaphunzitsa, kuti awachite m'dziko limene ndiwapatsa likhale laolao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iwe ukhale kuno ndi ine kuti ndikupatse malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene azitsatira mʼdziko limene ndiwapatse kuti alitenge.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iwe, uime kuno ndi Ine, ndinene ndi iwe malamulo onse, ndi malemba, ndi maweruzo, amene uziwaphunzitsa, kuti awacite m'dziko limene ndiwapatsa likhale lao lao.