Deuteronomy 5:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imene ija, ine ndidaaima pakati pa inu ndi Chauta ndi kumakuuzani mau a Chauta, chifukwa inu munkaopa moto, ndipo simudakwere phiri. Chauta adaati,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
(ndinalinkuima pakati pa Yehova ndi inu muja, kukulalikirani mau a Yehova; popeza munachita mantha chifukwa cha moto, osakwera m'phirimo) ndi kuti:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Pa nthawi imeneyo ine ndinayimirira pakati pa Yehova ndi inu kuti ndikuwuzeni mawu a Yehova, chifukwa inu munkachita mantha ndi moto ndipo simunakwere ku phiri). Ndipo Iye anati:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
(ndinalinkufma pakati pa Yehova ndi inu muja, kukulalikirani mau a Yehova; popeza munacita mantha cifukwa ca moto, osakwera m'phirimo) ndi kuti: