Deuteronomy 5:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usagwadire fano lililonse kapena kulipembedza, chifukwa Ine, Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, sindilola kuti wina apikisane nane. Ndimalanga amene adana nane. Ndimalanganso zidzukulu zao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndine Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate wao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
usazipembedzere izo, usazitumikire izo; cifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndine Mulungu wansanje, wakulanga ana cifukwa ca atate wao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai wa iwo amene akudana ndi Ine;