Deuteronomy 6:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono aŵa ndi malamulo, malangizo ndi zina zoyenera kuzitsata, zimene Chauta, Mulungu wanu, adandilamula kuti ndikuphunzitseni. Muzikatsata zonsezi m'dziko limene mudzaloŵa ndi kukhalamolo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo awa ndi malamulo, malemba, ndi maweruzo, amene Yehova Mulungu wanu analamulira kukuphunzitsani, kuti muziwachita m'dziko limene muolokerako kulilandira;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awa ndi malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene Yehova Mulungu wanu anandilamula kuti ndikuphunzitseni kuti mukawatsatire mʼdziko limene mukuwolokera Yorodani kuti mukalitenge,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo awa ndi malamulo, malemba, ndi maweruzo, amene Yehova Mulungu wanu analamulira kukuphunzitsani, kuti muziwacita m'dziko limene muolokerako kulilandira;