Deuteronomy 6:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
popeza kuti mukatero, mkwiyo wa Chauta udzakuyakirani ngati moto, ndipo udzakuwonongani kwathunthu, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, amene amakhala pakati panu, ndi Mulungu wansanje, salola kuti wina apikisane naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukuchotsani pankhope pa dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pakuti Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu, ndi Mulungu wansanje ndipo adzakukwiyirani kwambiri ndi kukuwonongani, kukufafanizani mʼdziko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukucotsani pankhope pa dziko lapansi.