Deuteronomy 6:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
nthaŵi zonse pamene muli moyo, inu ndi zidzukulu zanu. Muzikaopa Chauta, Mulungu wanu, ndipo muzikamvera malamulo ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsaniŵa, kuti pakutero mukakhale moyo nthaŵi yaitali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti muope Yehova Mulungu wanu, kusunga malemba ake onse ndi malamulo ake, amene ndikuuzani inu ndi ana anu, ndi zidzukulu zanu, masiku onse a moyo wanu, ndi kuti masiku anu achuluke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuti inuyo, ana anu, ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo mudzaope Yehova Mulungu wanu moyo wanu wonse posunga malangizo ndi malamulo ake onse amene ndinakupatsani inu kuti musangalale ndi moyo wautali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti muope Yehova Mulungu wanu, kusunga malemba ace onse ndi malamulo ace, amene ndikuuzani inu ndi ana anu, ndi zidzukulu zanu, masiku onse a moyo wanu, ndi kuti masiku anu acuruke.