Deuteronomy 6:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tikamasunga mokhulupirika zonse zimene Chauta Mulungu wathu watilamula, Iyeyo adzakondwera nafe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzakhala kwa ife chilungamo, ngati tisamalira kuchita malamulo awa onse pamaso pa Yehova Mulungu wathu, monga anatilamulira ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati tisamala kumvera malamulo onsewa pamaso pa Yehova Mulungu wathu monga momwe anatilamulira ife, chimenecho chidzakhala chilungamo chathu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzakhala kwa ife cilungamo, ngati tisamalira kucita malamulo awa onse pamaso pa Yehova Mulungu wathu, monga anatilamuliraife.