Deuteronomy 6:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo muziwaphunzitsa mwacangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.