Deuteronomy 7:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu wanu, adzakufikitsani m'dziko limene mukudzakhalamolo, ndipo mitundu ina yonse ya anthu adzaipirikitsa m'dzikomo. Iye adzachotsamo mitundu isanu ndi iŵiri ya anthu otchuka ndi amphamvu kupambana inu. Mitunduyo ndi iyi: Ahiti, Agirigasi, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene mumkako kulilandira likhale lanulanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikulu ndi yamphamvu yoposa inu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Yehova Mulungu wanu wakufikitsani mʼdziko limene mukukalowa ndi kulilanda ndi kuthamangitsa pamaso panu mitundu ya anthu iyi: Ahiti, Agirigasi, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi; yomwe ndi mitundu isanu ndi iwiri yayikulu ndi yamphamvu kuposa inu;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene mumkako kulilandira likhale lanu lanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigazi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikuru ndi yamphamvu yoposa inu;