Deuteronomy 7:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma onse amene amadana ndi Mulungu, adzaŵabwezera pakuŵaononga. Sadzamlekerera munthu wodana naye, koma adzamubwezera pakumlanga ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo awabwezera onse akudana ndi Iye, pamaso pao, kuwaononga; sachedwa naye wakudana ndi Iye, ambwezera pamaso pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iwo amene amamuda adzawabwezera powawononga pamaso pawo; sadzachedwa kuwabwezera iwo amene amadana naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo awabwezera onse akudana ndi iye, pamaso pao, kuwaononga; sacedwa naye wakudana ndi iye, ambwezera pamaso pace.