Deuteronomy 7:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati mumvera ndi kutsata mokhulupirika malamulo onse mwamvaŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzapitirirabe kusunga chipangano chake chimene adachita ndi inu, ndipo adzapitiriranso kukukondani, monga momwe adalonjezera makolo anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzakhala, chifukwa cha kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwachita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani chipangano ndi chifundo chimene analumbirira makolo anu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukamvera malamulo amenewa, ndi kusamala kuwatsata, ndiye kuti Yehova Mulungu wanu adzasunga pangano lake la chikondi chosasinthika ndi inu, monga analumbira kwa makolo anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzakhala, cifukwa ca kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwacita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani cipangano ndi cifundo cimene analumbirira makolo anu;