Deuteronomy 7:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumbukirani miliri yoopsa ija imene mudaiwona ndi maso anu. Mudaona zozizwitsa ndi zodabwitsa zomwe, ndiponso zinthu zazikulu zamphamvu. Zimenezi Chauta, Mulungu wanu, adazichita ndi dzanja lake lamphamvu, kuti akumasuleni. Anthu onse amene mumaŵaopaŵa, Chauta Mulungu wanu adzaŵaononga monga momwe adaonongera Aejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mayesero akulu maso anu anawapenya, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, zimene Yehova Mulungu wanu anakutulutsani nazo; Yehova Mulungu wanu adzatero nayo mitundu yonse ya anthu imene muwaopa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munadzionera nokha ndi maso anu mayesero aakulu, zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa, mphamvu yake yopanda malire imene Yehova Mulungu wanu anakutulutsirani. Yehova Mulungu adzachita zimenezo ndi anthu onse amene muwaopa tsopano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mayesero akuru maso anu anawapenya, ndi zizindikilo ndi zozizwa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, zimene Yehova Mulungu wanu anakuturutsani nazo; Yehova Mulungu wanu adzatero nayo mitundu yonse ya anthu imene muwaopa.