Deuteronomy 7:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudzatenthe mafano ao ofanizira milungu yao. Musadzakhumbire siliva kapena golide amene iwo adapangira mafanowo. Musadzatengeko zimenezi kuti mungagwe mu msampha, popeza kuti zimenezo zimamnyansa Chauta, Mulungu wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mafano osema a milungu yao muwatenthe ndi moto; musamasirira siliva ndi golide zili pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muwawotche pa moto mafano a milungu yawo. Musasirire siliva ndi golide amene ali pa mafanoyo. Musamutenge kuti akhale wanu chifukwa mukatero mudzakodwa naye ngati msampha, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa nazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mafano osema a milungu yao muwateothe ndi moto; musamasirira siliva ndi golidi ziri pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.