Deuteronomy 7:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kuti angadzaŵasokeretse kuŵachotsa kwa Chauta, Mulungu wanu, namakapembedza nawo milungu ina. Mukadzatero, Chauta adzakukwiyirani, ndipo adzakuwonongani mwamsanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata Ine, kuti atumikire milungu ina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuonongani msanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukadzatero, iwo adzasocheretsa ana anu aamuna kuti asanditsatire ndi kutumikira milungu ina. Motero Yehova adzakukwiyirani ndi kukuwonongani mwachangu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata Ine, kuti atumikire milungu yina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuonongani msanga.