Deuteronomy 7:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta adakukondani, ndipo adafunadi kusunga malumbiro amene adaachita ndi makolo anu. Nchifukwa chake adakupulumutsani ndi mphamvu zake, nakusandutsani mfulu, kukuchotsani m'dziko laukapolo kwa mfumu ya ku Ejipito ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m'nyumba ya akapolo, m'dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, chifukwa Yehova akukondani, ndi chifukwa cha kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma chifukwa chakuti Yehova anakukondani nasunga lumbiro lake limene analumbira kwa makolo anu. Ndi chifukwa chake anakutulutsani ndi mphamvu yake yopanda malire ndi kukupulumutsani ku dziko la ukapolo, kuchoka mʼmanja mwa Farao mfumu ya ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma Yehova anakuturutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m'nyumba ya akapolo, m'dzanja la Farao mfumu ya Aigupto, cifukwa Yehova akukondani, ndi cifukwa ca kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu.