Deuteronomy 8:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adakupatsani mana oti mudye, chakudya chimene makolo anu anali asanadyepo, pofuna kukutsitsani ndi kukuyesani, kuti pambuyo pake akuchitireni zokoma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene anakudyetsani m'chipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwe; kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akuchitireni chokoma potsiriza panu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anakupatsani mana kuti mudye mʼchipululu, zinthu zoti ngakhale makolo anu sanazidziwe, kuti akuchepetseni ndi kukuyesani ndipo kuti pa mapeto pake zikuyendereni bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene anakudyetsani m'cipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwa; kuti akucepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akucitireni cokoma potsiriza panu;