Deuteronomy 8:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumbukirani kuti amene amakupatsani mphamvu zoti mulemerere, ndi Chauta, Mulungu wanu. Adachita zimenezi kale popeza kuti sadafune kuphwanya chipangano chake chimene adachita ndi makolo anu, chimodzimodzi m'mene akuchitira lero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mukumbukire Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera chuma; kuti akhazikitse chipangano chake chimene analumbirira makolo anu, monga chikhala lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kumbukirani Yehova Mulungu chifukwa ndi amene amakupatsani mphamvu zopezera chuma chimenechi kuti atsimikize pangano limene analumbira kwa makolo anu, monga liliri lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mukumbukile Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera cuma; kuti akhazikitse cipangano cace cimene analumbirira makolo anu, monga cikhala lero lino.