Deuteronomy 8:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumbukirani m'mene Chauta, Mulungu wanu, adakutsogolerani m'chipululu, pa ulendo wa pa zaka zonse makumi anai zapitazi. Adakuvutani nakuyesani ndi zoŵaŵa, kuti adziŵe zimene zinali m'mitima mwanu, ndipo kuti aone ngati mudzamvera malamulo ake kapena ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumbukirani mmene Yehova Mulungu wanu anakutsogolerani njira yonse mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kukutsitsani ndi kukuyesani kuti adziwe chimene chinali mu mtima mwanu ngati mungathe kusunga malamulo ake kapena ayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mukumbukile njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'cipululu zaka izi makumi anai, kuti akucepetseni, kukuyesani, kudziwa cokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ace, kapena iai.