Deuteronomy 8:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukapanda kumvera Chauta, Mulungu wanu, mudzaonongeka monga momwe Chauta akuwonongera mitundu ina pamaso panu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga amitundu amene Yehova awaononga pamaso panu, momwemo mudzaonongeka; chifukwa cha kusamvera mau a Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga mitundu ina ya anthu imene Yehova anayiwononga pamaso panu, inunso mudzawonongedwa chifukwa chosamvera Yehova Mulungu wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga amitundu amene Yehova awaononga pamaso panu, momwemo mudzaonongeka; cifukwa ca kusamvera mau a Yehova Mulungu wanu.