Deuteronomy 9:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mvetsani inu Aisraele. Muli pafupi kuwoloka mtsinje wa Yordani ndi kukakhala m'dziko la anthu aakulu ndi amphamvu kupambana inu. Mizinda yao ndi ya malinga aatali ofika mpaka kumwamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Imvani Israele; mulikuoloka Yordani lero lino, kulowa ndi kulandira amitundu akulu ndi amphamvu akuposa inu, midzi yaikulu ndi ya malinga ofikira kuthambo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mvera Israeli. Watsala pangʼono kuwoloka Yorodani ndi kukathamangitsa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa iweyo, imene mizinda yake ndi ikuluikulu yokhala ndi makoma ofika mpaka kumwamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Imvani Israyeli; mulikuoloka Yordano lero lino, kulowa ndi kulandira amitundu akuru ndi amphamvu akuposa inu, midzi yaikuru ndi ya malinga ofikira kuthambo,