Deuteronomy 9:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zedi, patapita masiku makumi anaiwo, usana ndi usiku, Chauta adandipatsa miyala iŵiri ija, imene adaalembapo chipangano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, atatha masiku makumi anai usana ndi usiku, kuti Yehova anandipatsa magome awiriwo amiyala, ndiwo magome a chipangano.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakutha pa masiku makumi anayi usiku ndi usana, Yehova anandipatsa miyala iwiri, miyala ya pangano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, atatha masiku makumi anai usana ndi usiku, kuti Yehova anandipatsa magome awiriwo amiyala, ndiwo magome a cipangano,