Deuteronomy 9:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Chauta adandiwuza kuti, “Nyamuka tsika msanga, choka kuphiri kuno, chifukwa anthu ako aja udaŵatsogolera kuchokera ku Ejipitoŵa, adziipitsa kwambiri. Sadakhalire kupatuka pa zimene ndidaŵalamula kuti azichita, ndipo adzipangira fano losungunula.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa ine, Uka, fulumira kutsika kuno popeza anthu ako unawatulutsa m'Ejipitowa anadziipsa; anapatuka msanga m'njira ndinawalamulirayi; anadzipangira fano loyenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yehova anandiwuza, “Tsikako kuno msanga, chifukwa anthu ako aja unawatulutsa ku Iguptowa adziyipitsa. Iwo apatukapo mofulumira pa zimene ndinawalamulira ndipo adzipangira fano lachitsulo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa ine, Uka, fulumira kutsika kuno popeza anthu ako unawaturutsa m'Aigupto wa anadziipsa; anapatuka msanga m'njira ndinawalamulirayi; anadzipangira fano loyenga.