Deuteronomy 9:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo ndidatsika phiri, nditanyamula m'manja mwanga miyala iŵiri ija ya chipangano. M'phirimo munkatuluka malaŵi a moto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi phirilo linatentha ndi moto; ndi magome awiri a chipangano anali m'manja mwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ndinatembenuka ndi kutsika phiri moto ukanayakabe. Ndipo miyala iwiri ya pangano inali mʼmanja mwanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi phirilo linatentha ndi moto; ndi magome awiri a cipangano anali m'manja mwanga.