Deuteronomy 9:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nditayang'ana, ndidaona kuti inu mudachimwira Chauta, Mulungu wanu, pakudzipangira fano lachitsulo la mwanawang'ombe. Simudakhalire kuleka kusunga malamulo amene Chauta adakulamulani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinapenya, taonani, mudachimwira Yehova Mulungu wanu; mudadzipangira mwanawang'ombe woyenga; mudapatuka msanga m'njira imene Yehova adalamulira inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine poyangʼana ndinaona kuti inu munachimwira Yehova Mulungu wanu. Munadzipangira fano lowumbidwa ngati mwana wangʼombe. Inuyo munapatuka msanga kuchoka pa njira imene Yehova anakulamulirani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinapenya, taonani, mudacimwira Yehova Mulungu wanu; mudadzipangira mwana wa ng'ombe woyenga; mudapatuka msanga m'njira imene Yehova adalamulira inu.