Deuteronomy 9:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono masiku enanso makumi anai, usana ndi usiku, ndidagwada pamaso pa Chauta ndipo ndidapemphera. Sindidadye kapena kumwa kanthu kalikonse, chifukwa inuyo mudaachimwira Chauta ndikumkwiyitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova, monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku, osadya mkate osamwa madzi, chifukwa cha machimo anu onse mudachimwa, ndi kuchita choipacho pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono nthawi yomweyo ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usiku ndi usana. Sindinadye buledi kapena kumwa madzi chifukwa cha machimo onse amene munawachita, kuchita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kumukwiyitsa kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova, monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku, osadya mkate osamwa madzi, cifukwa ca macimo anu onse mudacimwa, ndi kucita coipaco pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wace.