Deuteronomy 9:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ake ngotchuka ndiponso ataliatali. Anthu amenewo ndi zidzukulu za Aanaki amene mukuŵadziŵa kale. Paja mudamva kale kuti amati, “Ndani angalimbane ndi zidzukulu za Anaki?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
anthu akulu ndi atalitali, ana a Aanaki, amene muwadziwa, amene munamva mbiri yao, ndi kuti, Adzaima ndani pamaso pa ana a Anaki?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwo ndi ataliatali, Aanaki! Ukudziwa za iwo ndipo unamvapo zikunenedwa kuti, “Ndani amene angalimbane ndi Aanaki?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
anthu akuru ndi atalitali, ana a Aanaki, amene muwadziwa, amene munamva mbiri yao, ndi kuti, Adzaima ndani pamaso pa ana a Anaki?