Deuteronomy 9:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chinthu chimene mudachipangacho, fano lachitsulo la mwanawang'ombelo, ndidaliponya pa moto. Tsono ndidaliphwanya pafupipafupi ndi kuliperapera, ndipo ndidataya phulusa lake ku mtsinje wotsika m'phiri uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinatenga tchimo lanu, mwanawang'ombe mudampangayo, ndi mumtentha ndi moto, ndi kumphwanya, ndi kumpera bwino kufikira atasalala ngati fumbi; ndipo ndinataya fumbi lake m'mtsinje wotsika m'phirimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiponso ndinatenga chinthu chanu choyipacho, mwana wangʼombe amene munapangayo, ndi kumuwotcha pa moto. Kenaka ndinamuphwanya ndi kumuperapera ndikukhala ngati fumbi ndipo ndinawaza fumbilo mu mtsinje umene unkayenda kuchokera mʼphiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinatenga cimo lanu, mwana wa ng'ombe mudampangayo, ndi kumtentha ndi moto, ndi kumphwanya, ndi kumpera bwino kufikira atasalala ngati pfumbi; ndipo ndinataya pfumbi lace m'mtsinje wotsika m'phirimo.