Deuteronomy 9:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Chauta atakutumani kuchokera ku Kadesi-Baranea kuti mupite kukalandira dziko limene adakupatsanilo, inu mudakana malamulo a Chauta, Mulungu wanu, ndipo simudamkhulupirire kapena kumumvera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Yehova anakutumizani kuchokera ku Kadesi-Baranea, ndi kuti Kwerani, landirani dziko limene ndakupatsani; munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu, osamkhulupirira, kapena kumvera mau ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova atakutulutsani ku Kadesi Barinea anati, “Pitani mukatenge dziko limene ndakupatsani.” Koma munawukira ulamuliro wa Yehova Mulungu wanu. Inu simunamukhulupirire kapena kumumvera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Yehova anakutumizani kucokera ku Kadesi Barinea, ndi kuti, Kwerani, landirani dziko limene ndakupatsani; munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu, osamkhulupirira, kapena kumvera mau ace.