Deuteronomy 9:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidapemphera motere, ndidati, “Inu Chauta, Ambuye athu, chonde musaŵaononge anthuŵa amene mudaŵasankha kuti akhale anuanu. Anthu ameneŵa mudaŵapulumutsa ndi ukulu wanu ndipo mudaŵatulutsa ku Ejipito ndi mphamvu zanu zazikulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinapemphera kwa Yehova ndi kuti, Yehova Mulungu, musaononga anthu anu ndi cholowa chanu, amene mudawaombola mwa ukulu wanu, amene munawatulutsa m'Ejipito ndi dzanja lamphamvu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinapemphera kwa Ambuye ndi kuti, “Haa Yehova Wamkulukulu, musawawononge anthu anu, chuma chanuchanu chimene munachipulumutsa ndi mphamvu yanu yayikulu ku Igupto ndi dzanja lanu la mphamvu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinapemphera kwa Yehova ndi kuti, Yehova Mulungu, musaononga anthu anu ndi colowa canu, amene mudawaombola mwa ukulu wanu, amene munawaturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu,