Deuteronomy 9:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kuti Aejipito aja angamadzanene kuti Inu simudathe konse kuŵaloŵetsa anthu anu m'dziko limene mudaŵalonjeza. Azidzanenanso kuti: Adaŵatulutsa anthuwo kuti akaŵaphe ku chipululu poti adadana nawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti linganene dziko limene mudatitulutsako, Popeza Yehova sanakhoze kuwalowetsa m'dziko limene adanena nao, ndi popeza anadana nao, anawatulutsa kuti awaphe m'chipululu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kupanda kutero, ndiye kuti anthu a ku dziko lija munatitulutsaku adzati, ‘Yehova anawatulutsa kuti akawaphe mʼchipululu popeza sanathe kukawalowetsa mʼdziko limene anawalonjeza ndipo anadana nawo.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti linganene dziko limene mudatiturutsako, Popeza Yehova sanakhoza kuwalowetsa m'dziko limene adanena nao, ndi popeza anadana nao, anawaturutsa kuti awaphe m'cipululu.