Deuteronomy 9:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma lero mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzakutsogolerani monga momwe umachitira moto wopsereza. Adzagonjetsa onse pamaso panu, kotero kuti mudzaŵapirikitsa ndi kuŵaononga mwamsanga monga Chauta adakulonjezerani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero mudziwe lero lino, kuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene aoloka pamaso panu ngati moto wonyeketsa; Iye adzawaononga, Iye adzawagwetsa pamaso panu; potero mudzawapirikitsa, ndi kuwaononga msanga, monga Yehova analankhula ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma khulupirira lero kuti Yehova Mulungu wako amene ali patsogolo pako ali ngati moto wonyeketsa. Adzawononga iwowo ndipo adzawagonjetsa iweyo ukuona. Pamenepo udzawathamangitsa ndi kuwakantha mwamsanga, monga momwe Yehova wakulonjezera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero mudziwe lero lino, kuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene aoloka pamaso panu ngati moto wonyeketsa; iye adzawaononga, iye adzawagwetsa pamaso panu; potero mudzawapitikitsa, ndi kuwaononga msanga, monga Yehova analankhula ndi inu.