Deuteronomy 9:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu wanu, ndiye adzakupirikitsirani iwowo. Ndiye inu musadzanene kuti wakuloŵetsani ndi kukupatsani dzikolo chifukwa cha zabwino zimene mwachita. Ai, Chauta akupirikitsirani anthu ameneŵa chifukwa choti iwowo ngoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamanena mumtima mwanu, atawapirikitsa pamaso panu Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Chifukwa cha chilungamo changa Yehova anandilowetsa kudzalandira dziko ili; pakuti Yehova awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Mulungu wako akadzawapirikitsa pamaso pako, usadzanene mu mtima mwako kuti, “Yehova wandibweretsa kuno kudzalanda dziko lino chifukwa cha kulungama kwanga.” Ayi, koma ndi chifukwa cha kuyipa kwa anthu amene Yehova ati awapirikitse pamaso pako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamanena mumtima mwanu, atawapitikitsa pamaso panu Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Cifukwa ca cilungamo canga Yehova anandilowetsa kudzalandira dziko ili; pakuti Yehova awapitikitsa pamaso panu cifukwa ca zoipa za amitundu awa.