Deuteronomy 9:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimene Chauta akukulolerani kuŵalanda dziko anthuwo, si chifukwa chakuti ndinu abwino ndi angwiro ai. Akuŵapirikitsa chifukwa iwowo ngoipa, ndiponso chifukwa choti Mulungu ndi wosunga lonjezo limene adachita ndi makolo anu Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Simulowa kulandira dziko lao chifukwa cha chilungamo chanu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sukalowa ndi kutenga dziko lawolo chifukwa cha kulungama kwako kapena kukhulupirika kwako koma chifukwa cha kuyipa kwa anthuwo. Yehova Mulungu wako awapirikitsa pamaso pako kuti akwaniritse zimene analumbira kwa makolo ako Abrahamu, Isake ndi Yakobo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Simulowa kulandira dziko lao cifukwa ca cilungamo canu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu cifukwa ca zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo.