Deuteronomy 9:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudziŵe tsono kuti Chauta sakukupatsani dziko labwinoli popeza kuti ndinu olungama ai. Inu ndinu anthu okanika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero mudziwe, kuti Yehova Mulungu wanu sakupatsani dziko ili lokoma mulilandire, chifukwa cha chilungamo chanu; pakuti inu ndinu mtundu wa anthu opulukira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono zindikira kuti si chifukwa cha kulungama kwako kuti Yehova Mulungu wako akukupatsa dziko labwinoli kuti ulitenge popeza ndiwe wokanika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero mudziwe, kuti Yehova Mulungu wanu sakupatsani dziko ili lokoma mulilandire, cifukwa ca cilungamo canu; pakuti inu ndinu mtundu wa aathu opulukira.