Deuteronomy 9:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musaiŵale m'mene mudakwiyitsira Chauta, Mulungu wanu, m'chipululu muja. Kuyambira tsiku lija mudatuluka ku Ejipito kuja, mpaka tsiku limene mudafika kuno, mwakhala mukuukira Chauta, Mulungu wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kumbukirani, musamaiwala, kuti munakwiyitsa Yehova Mulungu wanu m'chipululu; kuyambira tsikuli munatuluka m'dziko la Ejipito, kufikira munalowa m'malo muno munapikisana ndi Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumbukirani izi ndipo musayiwale mmene munaputira mkwiyo wa Yehova Mulungu mʼchipululu muja. Kuyambira tsiku limene munatuluka mu Igupto mpaka pamene munafika kuno, mwakhala owukira Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kumbukilani, musamaiwala, kuti munakwiyitsa Yehova Mulungu wanu m'cipululu; kuyambira tsikuli munaturuka m'dziko la Aigupto, kufikira munalowa m'malo muno munapiktsana ndi Yehova.