Ecclesiastes 1:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaaika mtima wanga pa kufunitsitsa kumvetsa bwino zonse zochitika pansi pano. Imeneyi ndi ntchito yolemetsa kwambiri imene Mulungu adatipatsa anthufe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimachitidwa pansi pa thambo; ntchito yovuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinayika mtima wanga pophunzira ndi kufunafuna mwa nzeru zinthu zonse zimene zimachitika pansi pa thambo. Ndi ntchito yolemetsa ndithu imene Mulungu anayipereka kwa anthu!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimacitidwa pansi pa thambo; nchito yobvuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.