Ecclesiastes 1:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaayesetsa kumvetsa kuti nzeru nchiyani, misala nchiyani, uchitsiru nchiyani. Koma ndidazindikira kuti kuterokonso kunali kungodzivuta chabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinadzipereka kuti ndithe kumvetsa kuti nzeru nʼchiyani, misala nʼchiyani, uchitsiru nʼchiyani, koma ndinazindikira ichi, kuti kuteronso nʼkungodzivuta chabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti icinso cingosautsa mtima.