Ecclesiastes 10:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ndiwe wodala iwe dziko, ngati mfumu yako ndi mwana wa mfulu. Ndiwe wodala ngati nduna zako zimachita phwando pa nthaŵi yabwino, kuti zikhale zamphamvu, osati kuti ziledzere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwai kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana wa aufulu, ndipo akalonga ako adya pa nthawi yoyenera akalimbe osati akaledzere ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wodala iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ndi mwana wolemekezeka ndipo atsogoleri ako amadya pa nthawi yake, kuti apeze mphamvu osati kuti aledzere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwai kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana wa aufulu, ndipo akalonga ako adya pa nthawi yoyenera akalimbe osati akaledzere ai.