Ecclesiastes 10:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale mumtima mwako usamainyoza mfumu. Ngakhale m'chipinda mwako momwe usamatukwana wolemera. Mwina kambalame kamumlengalenga kapena kachilombo kena kouluka nkukumvera, kenaka nkukaulula zonse kwa amene umaŵanenawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'chipinda chogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo chouluka ndi mapiko chidzamveketsa zonenazo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Usanyoze mfumu ngakhale mu mtima mwako, kapena kutukwana munthu wachuma mʼchipinda chako, pakuti mbalame yamlengalenga itha kutenga mawu ako nʼkukafotokoza zomwe wanena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'cipinda cogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo couluka ndi mapiko cidzamveketsa zonenazo.