Ecclesiastes 11:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu akakhala wa zaka zambiri, mlekeni akondwerere zaka zonsezo. Koma azikumbukira kuti masiku otsatira imfa yake ndi ochuluka koposa. Zonse zikudzazi nzopanda phindu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inde, munthu akakhala ndi moyo zaka zambiri, akondwere ndi zonsezo; koma akumbukire masiku amdima kuti adzachuluka. Zonse zilinkudza zili zachabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu akakhala wa zaka zambiri, mulekeni akondwerere zaka zonsezo, koma iye azikumbukira masiku a mdima, pakuti adzakhala ochuluka. Chilichonse chimene chikubwera ndi chopanda phindu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inde, munthu akakhala ndi moyo zaka zambiri, akondwere ndi zonsezo; koma akumbukire masiku amdima kuti adzacuruka. Zonse zirinkudza ziri zacabe.