Ecclesiastes 12:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzaopa kukwera pa malo apamwamba, ndipo nkuyenda komwe kudzakhala koopsa. Kumutu kudzangoti mbu, udzalephera nkuyenda kodziguza komwe, ndipo chilakolako chilichonse chidzakuthera. Tonse tikupita kwathu kokakhala mpaka muyaya, ndipo titapita kudzakhala kulira m'miseu yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsa; katungurume adzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Imeneyi ndiyo nthawi imene anthu amaopa kupita kumalo okwera, amaopa kuyenda mʼmisewu; Mutu umatuwa kuti mbuu, amayenda modzikoka ngati ziwala ndipo chilakolako chimatheratu. Nthawi imeneyo munthu amapita ku nyumba yake yamuyaya ndipo anthu olira maliro amayendayenda mʼmisewu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsya; mciu nudzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja;