Ecclesiastes 12:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chakuti Mlalikiyo anali waluntha, adaphunzitsa anthu zambiri. Ankasinkhasinkha, kufufuzafufuza ndi kulongosola malangizo mosamala kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anatchera makutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mlaliki sanali wozindikira zinthu kokha ayi, komanso ankaphunzitsa anthu. Iye ankasinkhasinkha ndi kufufuzafufuza ndi kulemba mwadongosolo miyambi yambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anachera makutu nafunafuna nalongosolamiyambiyambiri.