Ecclesiastes 2:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi zina mumtima mwangamu ndinkati, “Ah! Tsopano ndiyesepo zokondweretsa, ndidzisangalatse.” Koma ai, zimenezinso zinali zopanda phindu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi chimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, ichinso ndi chabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Tsopano ndiyese zosangalatsa kuti ndipeze zomwe ndi zabwino.” Koma izi zinaonekanso kuti ndi zopandapake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi cimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, icinso ndi cabe.