Ecclesiastes 2:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidayamba kulingalira zonse zimene ndidazichita, ntchito zolemetsa zonse zimene ndidazigwira, nkuwona kuti zonsezo zinali zopanda phindu. Kunali kungodzivuta chabe. Ndithu panalibe choti nkupindulapo pa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene ndinayamba kuyangʼanayangʼana zonse zimene ndinachita ndi manja anga, ndi zimene ndinazivutikira kuti ndizipeze, zonsezi zinali zopandapake; kungodzivuta chabe, palibe chomwe ndinapindula pansi pano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi nchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zacabecabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.