Ecclesiastes 2:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo ndidayesanso kulingalira kuti kwenikweni nzeru nchiyani, misala nchiyani, uchitsiru nchiyani. Kodi munthu wodzaloŵa ufumu tsopanoyo angapose bwanji mnzake adapita uja? Nzokhazokhazo zomwe ameneyo adazichita kale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinatembenuka kukayang'ana nzeru ndi misala ndi utsiru; pakuti yemwe angotsata mfumu angachite chiyani? Si chomwe chinachitidwa kale.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka maganizo anga anayamba kulingalira zakuti nzeru nʼchiyani, komanso kuti misala ndi uchitsiru nʼchiyani. Kodi munthu wodzalowa ufumu tsopanoyo angachite chiyani choposa chimene chinachitidwa kale?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinatembenuka kukayang'ana nzeru ndi misala ndi utsiru; pakuti yemwe angotsata mfumu angacite ciani? Si comwe cinacitidwa kale.