Ecclesiastes 2:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inde munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo, pamene chitsiru chimayenda m'chimbulimbuli. Komabe ndidazindikira kuti zomwe zagwera winayo, mnzakeyonso zimamgwera zomwezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wanzeru maso ake ali m'mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo, pamene chitsiru chimayenda mʼchimbulimbuli; koma ndinazindikira kuti chomwe chimawachitikira onsewo ndi chimodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wanzeru maso ace ali m'mutu wace, koma citsiru ciyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti comwe ciwagwera onsewo ndi cimodzi.