Ecclesiastes 2:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Kani zimene zimagwera chitsiru nanenso zidzandigwera zomwezo! Nanga tsono ineyo nzeru zambiri chotere nzanji?” Pamenepo ndidaona kuti zimenezinso nzopanda phindu!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Chomwe chigwera chitsiru nanenso chindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti ichinso ndi chabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo ndinalingalira mu mtima mwanga, “Zochitikira chitsiru zidzandichitikiranso ine. Nanga tsono phindu langa nʼchiyani pakukhala wanzeru?” Ndinati mu mtima mwanga, “Ichinso ndi chopandapake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Comwe cigwera citsiru nanenso cindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti icinso ndi cabe.