Ecclesiastes 2:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti munthu wanzeru, pamodzi ndi chitsiru chomwe, onsewo sakumbukika nthaŵi yaitali, pokhala kuti pa masiku akutsogolo, onsewo adzaiŵalika. M'mene chimafera chitsiru ndi m'menenso amafera munthu wanzeru.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti wanzeru saposa chitsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo. Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati chitsirutu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti munthu wanzeru, pamodzinso ndi chitsiru sadzakumbukiridwa nthawi yayitali; mʼmasiku amʼtsogolo awiriwo adzayiwalika. Mmene chimafera chitsiru ndi mmenenso amafera wanzeru!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti wanzerusaposa citsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo, Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati citsirutu.