Ecclesiastes 2:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero moyo wanga ndidaipidwa nawo, chifukwa chakuti zonse zochitika pansi pano zimandimvetsa chisoni. Ndithudi, zonsezo nzopandapake, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ndinada moyo; pakuti ntchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero ndinadana nawo moyo chifukwa ntchito zimene zimagwiridwa pansi pano ndi zosautsa kwa ine. Ntchito zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ndinada moyo; pakuti nchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi cabe ndi kungosautsa mtima.