Ecclesiastes 2:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndani amadziŵa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala womalamulira zonse zimene ndidazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Zimenezinso nzopanda phindu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndani adziwa ngati adzakhala wanzeru pena chitsiru? Koma adzalamulira ntchito zanga zonse ndinasauka nazo, ndi kuzigwira mwanzeru kunja kuno. Ichinso ndi chabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndani amadziwa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala wolamulira zonse zimene ndinazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Izinso ndi zopandapake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndani adziwa ngati adzakhala wanzeru pena citsiru? Koma adzalamulira nchito zanga zonse ndinasauka nazo, ndi kuzigwira mwanzeru kunja kuno. Icinso ndi cabe.